2 Kings 7:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono phungu wokhulupirika wa mfumu adafunsa munthu wa Mulungu uja kuti, “Ngakhale Chauta mwiniwake atachita kutikhuthulira mvula yochuluka chotani, zoterezi nkuchitika ngati?” Koma Elisa adati, “Ndithu udzaziwona zimenezo ndi maso ako, koma iweyo sudzazilaŵa.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo kazembe amene mfumu ankatsamira pa dzanja lake anamyankha munthu wa Mulungu, nati, Taonani, Yehova angachite mazenera m'mwamba chidzachitika ichi kodi? Nati iye, Taona, udzachiona ndi maso ako, koma iwe sudzadyako ai.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mtsogoleri amene mfumu inkamudalira anati kwa munthu wa Mulungu, “Taona, ngakhale Yehova atatsekula zipata zakumwamba, kodi zimenezi zingachitikedi?” Elisa anamuyankha kuti, “Taona, iweyo udzaziona zimenezi ndi maso ako, koma sudzadyako kanthu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo kazembe amene mfumu adafotsamira pa dzanja lace anamyankha munthu wa Mulungu, nati, Taonani, Yehova angacite mazenera m'mwamba cidzacitika ici kodi? Nati iye, Taona, udzaciona ndi maso ako, koma iwe sudzadyako ai.