2 Kings 7:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthaŵi imeneyo panali anthu akhate anai amene ankakhala pa chipata. Iwowo adayamba kufunsana kuti, “Chifukwa chiyani tikungotambalala pano kumangodikira imfa?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma polowera pa chipata panali amuna anai akhate, nanenana wina ndi mnzake, Tikhaliranji kuno mpaka kufa?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono pa chipata cholowera mu mzinda wa Samariya pankakhala anthu anayi akhate. Iwo anayankhulana kuti, “Chifukwa chiyani tikungokhala pano kudikira kufa?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma polowera pa cipata panali amuna anai akhate, nanenana wma ndi mnzace, Tikhaliranji kuno mpaka kufa?