2 Kings 7:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tikati tiyeni tiloŵe mumzindamu, njala ili m'menemo kumene, ndiye tikaferamo. Komanso tikangotambalala pompano, tifabe. Tsono tiyeni tingopita ku zithando za Asiriya. Akatileka ndi moyo, chabwino, koma akatipha, palibe kanthu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tikati, Tilowe m'mudzi, m'mudzi muli njala, tidzafa m'mwemo; tikakhala pompano, tidzafanso. Tiyeni tsono, tigwe ku misasa ya Aaramu; akatisunga ndi moyo, tidzakhala ndi moyo; akatipha, tangokufa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngati tinganene kuti, ‘Tidzalowa mu mzinda,’ njala ili mu mzindamo ndipo tidzafa. Ndipo ngati tikhalebe pano, tidzafa ndithu. Choncho tiyeni tipite ku msasa wa Aaramu ndi kukadzipereka. Ngati sakatipha, tidzakhala ndi moyo, ngati akatipha, basi tikafa.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tikati, Tilowe m'mudzi, m'mudzi muli njala, tidzafa m'mwemo; tikakhala pompano, tidzafanso. Tiyeni tsono, tigwe ku misasa ya Aaramu; akatisunga ndi moyo, tidzakhala ndi moyo; akatipha, tangokufa.