2 Kings 7:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero adanyamuka ndi chisisira kupita ku zithando za Asiriya. Koma atafika ku malire a zithando za Asiriya, adaona kuti panalibe munthu ndi mmodzi yemwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nanyamuka iwo kuli sisiro kukalowa ku misasa ya Aaramu; koma pofika polekezera pake pa misasa ya Aaramu, taonani, panalibe munthu pomwepo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo ananyamuka ndi kachisisira kupita ku msasa wa Aaramu. Atafika mʼmalire a msasa, taonani, sanapeze munthu ndi mmodzi yemwe,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nanyamuka iwo kuli sisiro kukalowa ku misasa ya Aaramu; koma pofika polekezera pace pa misasa ya Aaramu, taonani, panalibe munthu pomwepo.