2 Kings 7:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho akhate aja atafika ku malire a zithandozo, adakaloŵa mu hema limodzi, ndipo adadya ndi kumwa. Atatero adatengako siliva, golide ndi zovala, nakazibisa. Pambuyo pake adabwerera nakaloŵa mu hema linanso, natengamo zinthu, nkukazibisanso.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pofika akhate ao polekezera pa misasa, analowa m'hema mmodzi, nadya namwa, natengako siliva ndi golide ndi zovala, namuka, nazibisa; nabwerera, nalowa m'hema mwina, natengako, namuka, nazibisa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu akhate aja atafika mʼmalire mwa msasa analowa mʼtenti imodzi. Anadya ndi kumwa, natenga siliva, golide ndi zovala ndipo anachoka kupita kukazibisa. Atabwerera anakalowa mʼtenti ina ndipo anatenga zinthu mʼmenemo nakazibisanso.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pofika akhate ao polekezera pa misasa, analowa m'hema mmodzi, nadya namwa, natengako siliva ndi golidi ndi zobvala, namuka, nazibisa; nabwerera, nalowa m'hema mwina, natengako, namuka, nazibisa.