2 Kings 7:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kenaka akhate aja adayamba kuuzana kuti, “Ife sitikuchita bwinotu pamenepa. Lero ndilo tsiku limene tili ndi uthenga wabwino kwambiri! Tikakhala chete ndi kumadikira mpaka m'maŵa, tidzalangidwa. Nchifukwa chake tsono tiyeni tikauze nduna za mfumu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo ananenana wina ndi mnzake, Sitilikuchita bwino ife; tsiku lino ndilo tsiku la uthenga wabwino, ndipo tilikukhala chete; tikachedwa kufikira kwacha, mphulupulu yathu idzatipeza; tiyeni tsono, timuke, tifotokozere a m'nyumba ya mfumu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka akhate aja anawuzana kuti, “Ife sitikuchita bwino. Lero ndi tsiku la uthenga wabwino ndipo tikungokhala chete. Tikadikira mpaka kucha, tidzalangidwa. Tiyeni msanga tikafotokoze zimenezi ku nyumba yaufumu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo ananenana wina ndi mnzace, Sitirikucita bwino ife; tsiku lino ndilo tsiku la uthenga wabwino, ndipo tirikukhala cete; tikacedwa kufikira kwaca, mphulupulu yathu idzatipeza; tiyeni tsono, timuke, tifotokozere a m'nyumba ya mfumu.