2 Kings 8:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndiye kuti Elisa anali atauza mai amene adaamuukitsira mwana wake uja kuti, “Nyamuka upite pamodzi ndi a pabanja pako, ukakhale nawo kulikonse kumene ungathe kukakhala, pakuti Chauta akubweretsa pa dziko njala ya zaka zisanu ndi ziŵiri.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Elisa ananena ndi mkazi uja adamuukitsira mwana wake, kuti, Nyamuka, numuke iwe ndi banja lako, nugonere komwe ukaone malo; pakuti Yehova waitana njala, nidzagwera dziko zaka zisanu ndi ziwiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Elisa anawuza mayi amene anamuukitsira mwana wake kuti, “Choka kuno pamodzi ndi banja lako ndipo ukakhale kulikonse ukufuna, chifukwa Yehova akubweretsa njala ya zaka zisanu ndi ziwiri mʼdziko muno.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Elisa ananena ndi mkazi uja adamuukitsira mwana wace, kuti, Nyamuka, numuke iwe ndi banja lako, nugonere komwe ukaone malo; pakuti Yehova waitana njala, nidzagwera dziko zaka zisanu ndi ziwiri.