2 Kings 8:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo Hazaele adafunsa kuti, “Kodi kapolo wanune amene ndine wonyozeka ngati galu, ndingathe bwanji kuchita zinthu zazikulu zoterezi?” Elisa adayankha kuti, “Chauta wandiwonetsa kuti iweyo udzakhala mfumu ya Asiriya.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nati Hazaele, Koma nanga kapolo wanu ali chiyani, ndiye galu, kuti akachite chinthu chachikulu ichi? Nayankha Elisa, Yehova wandionetsa kuti udzakhala mfumu ya pa Aramu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Hazaeli anati, “Kodi kapolo wanune, amene ndine wonyozeka ngati galu, ndingathe bwanji kuchita chinthu chachikulu chotere?” Elisa anayankha kuti, “Yehova wandionetsa kuti iwe udzakhala mfumu ya ku Aramu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nati Hazaeli, Koma nanga kapolo wanu ali ciani, ndiye garu, kuti akacite cinthu cacikuru ici? Nayankha Elisa, Yehova wandionetsa kuti udzakhala mfumu ya pa Aramu.