2 Kings 8:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pomwepo Hazaeleyo adasiyana naye Elisa, napita kwa mbuyake. Mbuyakeyo adamufunsa kuti, “Kodi Elisa wakuuza zotani?” Hazaele adayankha kuti, “Inuyo muchira ndithu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anachoka kwa Elisa, nadza kwa mbuye wake; ameneyo ananena naye, Anakuuza chiyani Elisa? Nati iye, Anandiuza kuti mudzachira ndithu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Hazaeli anasiyana ndi Elisa ndi kubwerera kwa mbuye wake. Beni-Hadadi atafunsa kuti, “Elisa wakuwuza chiyani?” Hazaeli anayankha kuti, “Elisa wandiwuza kuti inu mudzachira ndithu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anacoka kwa Elisa, nadza kwa mbuye wace; ameneyo ananena naye, Anakuuza ciani Elisa? Nati iye, Anandiuza kuti mudzacira ndithu.