2 Kings 8:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Yehoramuyo ankatsata makhalidwe oipa a mafumu a ku Aisraele, monga m'mene linkachitira banja la Ahabu, pakuti adaakwatira mwana wa Ahabu. Tsono ankachita zoipa zili zonse pamaso pa Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nayenda m'njira ya mafumu a Israele, m'mene inachitira nyumba ya Ahabu; pakuti mkazi wake ndiye mwana wa Ahabu, nachita iye choipa pamaso pa Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anatsatira khalidwe la mafumu a ku Israeli, monga mmene linachitira banja la Ahabu, popeza iye anakwatira mwana wa Ahabu. Yehoramu anachita zoyipa pamaso pa Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nayenda m'njira ya mafumu a Israyeli, m'mene inacitira nyumba ya Ahabu; pakuti mkazi wace ndiye mwana wa Ahabu, nacita iye coipa pamaso pa Yehova.