2 Kings 8:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Komabe Chauta sadafune kuwononga Yuda, chifukwa cha Davide mtumiki wake, popeza kuti Chauta adaalonjeza kuti adzampatsa nyale Davide ndi zidzukulu zake mpaka muyaya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Yehova sanafune kuononga Yuda, chifukwa cha Davide mtumiki wake monga adamuuza, kuti adzampatsa nyali ya kwa ana ake kosalekeza.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Komabe, chifukwa cha mtumiki wake Davide, Yehova sanafune kuwononga Yuda popeza Yehova analonjeza Davide kuti adzamupatsa nyale pamodzi ndi zidzukulu zake mpaka muyaya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Yehova sanafuna kuononga Yuda, cifukwa ca Davide mtumiki wace monga adamuuza, kuti adzampatsa nyali ya kwa ana ace kosalekeza.