2 Kings 8:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero maiyo adanyamuka, ndipo adachitadi monga momwe munthu wa Mulungu uja adaanenera. Adapita pamodzi ndi a pabanja pake, nakakhala nawo ku dziko la Afilisti zaka zisanu ndi ziŵiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nanyamuka mkaziyo, nachita monga mwa mau a munthu wa Mulunguyo, namuka ndi banja lake, nagonera m'dziko la Afilisti zaka zisanu ndi ziwiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mayiyo ananyamuka nachita zimene munthu wa Mulungu ananena. Iye pamodzi ndi banja lake anachoka nakakhala ku dziko la Afilisti zaka zisanu ndi ziwiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nanyamuka mkaziyo, nacita monga mwa mau a munthu wa Mulunguyo, namuka ndi banja lace, nagonera m'dziko la Afilisti zaka zisanu ndi ziwiri.