2 Kings 8:21 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Yehoramu adapita ku Zairi pamodzi ndi magaleta ake onse ankhondo. Adanyamuka usiku nakaŵakantha Aedomu amene adaamzinga iyeyo pamodzi ndi atsogoleri a magaleta ake. Ankhondo ake onse adathawa napita kwao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo Yoramu anaoloka kunka ku Zairi, ndi magaleta ake onse pamodzi naye; nauka iye usiku, nakantha Aedomu akumzinga ndi nduna za magaleta, nathawira anthu kwa mahema ao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Yehoramu anapita ku Zairi pamodzi ndi magaleta ake onse. Ndipo iye anakantha Aedomu amene anamuzungulira pamodzi ndi oyendetsa magaleta ake usiku. Koma ankhondo ake anathawa napita ku misasa yawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo Yoramu anaoloka kumka ku Zairi, ndi magareta ace onse pamodzi naye; nauka iye usiku, nakantha Aedomu akumzinga ndi nduna za magareta, nathawira anthu ku mahema ao.