2 Kings 8:28 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono mfumu Ahaziya adapita pamodzi ndi Yoramu, mwana wa Ahabu, kuti akamenyane nkhondo ndi Hazaele, mfumu ya ku Siriya, ku Ramoti ku Giliyadi. Kumeneko Asiriya adalasa Yoramu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anamuka Yoramu mwana wa Ahabu kukathira nkhondo pa Hazaele mfumu ya Aramu ku Ramoti Giliyadi; ndi Aaramu analasa Yoramu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ahaziya anapita pamodzi ndi Yoramu mwana wa Ahabu kukachita nkhondo ndi Hazaeli mfumu ya Aramu ku Ramoti Giliyadi. Aaramu anavulaza Yoramu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anamuka Yoramu mwana wa Ahabu kukathira nkhondo pa Hazaeli mfumu ya Aramu ku Ramoti Gileadi; ndi Aaramu analasa Yoramu.