2 Kings 8:29 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Yoramuyo adabwerera napita ku Yezireele, kuti akamchiritse mabala amene Asiriya adaamlasa ku Rama, pamene ankamenyana ndi Hazaele mfumu ya ku Siriya. Motero Ahaziya, mwana wa Yehoramu, mfumu ya ku Yuda, adapita ku Yezireele kukazonda Yoramu mwana wa Ahabu, chifukwa chakuti ankadwala.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mfumu Yoramu anabwera kuti ampoletse m'Yezireele mabalawo adamkantha Aaramu ku Rama, polimbana naye Hazaele mfumu ya Aramu. Natsikirako Ahaziya mwana wa Yehoramu mfumu ya Yuda kukamuona Yoramu mwana wa Ahabu m'Yezireele, pakuti anadwala.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho mfumu Yoramu inabwerera ku Yezireeli kuti ikachire mabala ake amene Aaramu anamuvulaza ku Rama pa nkhondo yake ndi Hazaeli mfumu ya Aramu. Tsono Ahaziya mwana wa Yehoramu mfumu ya ku Yuda anapita ku Yezireeli kuti akamuone Yoramu mwana wa Ahabu, popeza nʼkuti akudwala.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mfumu Yoramu anabwera kuti ampoletse m'Yezreeli mabalawo adamkantha Aaramu ku Rama, polimbana naye Hazaeli mfumu ya Aramu, Natsikirako Ahaziya mwana wa Yehoramu mfumu ya Yuda kukamuona Yoramu mwana wa Ahabu m'Yezreeli, pakuti anadwala.