2 Kings 8:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Atafika kwa mfumu, adapeza mfumuyo ikulankhula ndi Gehazi, mtumiki wa munthu wa Mulungu uja, nimafunsa kuti, “Tandiwuza zonse zikuluzikulu zimene Elisa wachita.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma mfumu inalikulankhula ndi Gehazi mnyamata wa munthu wa Mulungu, ndi kuti, Ndifotokozere zazikulu zonse Elisa wazichita.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo mfumu inkayankhula ndi Gehazi, mtumiki wa munthu wa Mulungu kuti, “Tandiwuza zinthu zikuluzikulu zimene Elisa wachita.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma mfumu inalikulankhula ndi Gehazi mnyamata wa munthu wa Mulungu, ndi kuti, Ndifotokozere zazikuru zonse Elisa wazicita.