2 Kings 8:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene mtumikiyo ankauza mfumuyo m'mene Elisa adaukitsira anthu akufa, mkazi uja, amene mwana wake Elisa adamuukitsira, adadzafunsa mfumu za nyumba yake ndi munda wake. Pamenepo Gehazi adati, “Inu mbuyanga mfumu, pano pali mai, ndipo mwana wake ndi uyu amene Elisa adamuukitsa.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali, alimkufotokozera mfumu m'mene adamuukitsira wakufayo, taonani, mkaziyo adamuukitsira mwana wake ananena za nyumba yake ndi munda wake kwa mfumu. Nati Gehazi, Mbuye wanga mfumu, suyu mkaziyo, suyu mwana wake Elisa anamuukitsayo?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene Gehazi ankayiwuza mfumuyo momwe Elisa anaukitsira anthu akufa, mayi amene mwana wake Elisa anamuukitsa kwa akufayo analowa kudzafunsa mfumu za nyumba yake ndi munda wake. Gehazi anati, “Mbuye wanga mfumu, mayi wake ndi uyu ndipo mwana wakeyo ndi uyu amene Elisa anamuukitsa kwa akufa.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunali, alimkufotokozera mfumu m'mene adamuukitsira wakufayo, taonani, mkaziyo adamuukitisira mwana wace ananena za nyumba yace ndi munda wace kwa mfumu. Nati Gehazi, Mbuye wanga mfumu, suyu mkaziyo, suyu mwana wace Elisa anamuukitsayo?