2 Kings 8:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mfumu itamufunsa maiyo, iyeyo adaifotokozera kuti Elisa adaukitsadi mwana wake. Choncho mfumu ija idamuikira nduna maiyo niiwuza kuti, “Umbwezere zonse zimene zidaali zake, pamodzi ndi phindu lonse lochokera ku zokolola za kumunda kwake, kuyambira tsiku limene adachoka mpaka tsopano lino.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pofunsa mfumu, mkaziyo anaisimbira. Pamenepo mfumu anamuikira mdindo, ndi kuti, Bwezetsa zake zonse ndi zipatso zonse za m'munda, chichokere iye m'dziko mpaka lero lino.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mfumu inafunsa mayiyo za nkhaniyi ndipo iye anayifotokozera mfumuyo. Ndipo mfumu inasankha munthu woti ayendetse nkhani yake ndipo inati, “Mubwezereni zonse zimene zinali zake, kuphatikizapo phindu lonse lochokera mʼmunda wake, kuyambira tsiku limene anachoka mpaka tsopano lino.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pofunsa mfumu, mkaziyo anaisimbira. Pamenepo mfumu anamuikira mdindo, ndi kuti, Bwezetsa zace zonse ndi zipatso zonse za m'munda, cicokere iye m'dziko mpaka lero lino.