2 Kings 8:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero Hazaele adapita kukakumana ndi mneneri Elisa, atasenzetsa ngamira 40 mphatso ndi zinthu zokoma zosiyanasiyana za ku Damasiko. Atafika, adakaima pamaso pa Elisa, munthu wa Mulungu uja, nati, “Munthu wanu Benihadadi, mfumu ya ku Siriya, wandituma kuti ndikufunseni kuti, kodi ati adzachira?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Namuka Hazaele kukakomana naye, napita nacho chaufulu, ndicho cha zokoma zonse za m'Damasiko, zosenza ngamira makumi anai, nafika naima pamaso pake, nati, Mwana wanu Benihadadi mfumu ya Aramu, wandituma ine kwa inu, ndi kuti, Kodi ndidzachira nthenda iyi?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Hazaeli anapita kukakumana ndi Elisa, atasenzetsa ngamira 40 mphatso za zinthu zosiyanasiyana zabwino kwambiri za ku Damasiko. Iye analowa mʼnyumba ya Elisa ndi kuyima pamaso pake, ndipo anati, “Mwana wanu Beni-Hadadi wandituma kuti ndidzakufunseni kuti, ‘Kodi ndidzachira matenda angawa?’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Namuka Hazaeli kukakomana naye, napita naco caufulu, ndico ca zokoma zonse za m'Damasiko, zosenza ngamila makumi anai, nafika naima pamaso pace, nati, Mwana wanu Benihadadi mfumu ya Aramu, wandituma ine kwa inu, ndi kuti, Kodi ndidzacira nthenda iyi?