2 Kings 9:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Yehu atatuluka kubwerera kwa atsogoleri anzake aja, iwo adamufunsa kuti, “Kodi nkwabwino? Wamsala uja anadzatani kwa inu?” Yehu adayankha kuti “Ai, mukumdziŵa munthu wotere ndi zolankhula zake zomwe.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehu anatulukira kwa anyamata a mbuye wake, nanena naye wina, Mtendere kodi? Anakudzera chifukwa ninji wamisala uyu? Nanena nao, Mumdziwa munthuyo ndi makambidwe ake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehu atatuluka kupita kumene kunali atsogoleri anzake, mmodzi mwa iwo anamufunsa kuti, “Kodi zonse zili bwino? Kodi munthu wamisala uja anabwera kudzatani kwa iwe?” Yehu anayankha kuti, “Iwe ukumudziwa munthu uja ndiponso ukudziwa zomwe amayankhula.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yehu anaturukira kwa anyamata a mbuye wace, nanena naye wina, Mtendere kodi? anakudzera cifukwa ninji wamisala uyu? Nanena nao, Mumdziwa munthuyo ndi makambidwe ace.