2 Kings 9:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero Yehu, mwana wa Yehosafati, mdzukulu wa Nimisi, adachita chiwembu mfumu Yoramu. Pomwe zinkachitika zimenezi, nkuti Yoramu pamodzi ndi Aisraele onse akudikira Hazaele mfumu ya Asiriya ku Ramoti-Giliyadi, kuti amenyane naye nkhondo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Motero Yehu mwana wa Yehosafati mwana wa Nimisi anapandukira Yoramu. Tsono Yoramu atalindira ku Ramoti Giliyadi, iye ndi Aisraele onse, chifukwa cha Hazaele mfumu ya Aramu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Yehu mwana wa Yehosafati, mwana wa Nimisi, anachitira chiwembu Yoramu. (Nthawi imeneyi nʼkuti Yoramu ndi Aisraeli onse akuteteza Ramoti Giliyadi kwa Hazaeli mfumu ya ku Aramu,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Motero Yehu mwana wa Yehosafati mwana wa Nimsi anapandukira Yoramu. Tsono Yoramu atalindira ku Ramoti Gileadi, iye ndi Aisrayeli onse, cifukwa ca Hazaeli mfumu ya Aramu;