2 Kings 9:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma nthaŵiyo mfumu Yoramu anali atabwerera ku Yezireele, kuti akachire mabala amene adamlasa Asiriya aja pa nthaŵi imene ankamenyana nkhondo ndi Hazaele uja. Tsono Yehu adauza atsogoleri ankhondo anzake aja kuti, “Ngati mufuna kuti ndikhale mfumu, musalole ndi mmodzi yemwe kuti achoke mumzinda muno, kuti akanene nkhani zimenezi ku Yezireele.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
koma mfumu Yoramu adabwera ku Yezireele ampoletse mabala ake anamkantha Aaramu, muja adalimbana naye Hazaele mfumu ya Aramu. Nati Yehu, Ukatero mtima wanu, asapulumuke mmodzi yense kutuluka m'mudzi kukafotokozera m'Yezireele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
koma nʼkuti Yoramu atabwerera ku Yezireeli kuti akachire mabala amene Aaramu anamuvulaza pa nkhondo ndi Hazaeli mfumu ya ku Aramu.) Yehu anati, “Ngati mukugwirizana nazo zimenezi, wina aliyense asatuluke mu mzinda muno kupita kukafotokoza nkhaniyi ku Yezireeli.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
koma mfumu Yoramu adabwera ku Yezreeh ampoletse mabala ace anamkantha Aaramu, muja adalimbana naye Hazaeli mfumu ya Aramu. Nati Yehu, Ukatero mtima wanu, asapulumuke mmodzi yense kuturuka m'mudzi kukafotokozera m'Yezreeli.