2 Kings 9:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Munthu wokwera pa kavalo uja adapita kukakumana nawo nati, “Mfumu ikufunsa kuti, ‘Kodi ndi zamtendere?’ ” Yehu adayankha kuti, “Kodi iweyo nkhani ya mtendere uli nayo chiyani? Tiye, uzinditsata pambuyo.” Mlonda uja adakanena kwa mfumu Yoramu kuti, “Wamthenga uja wakafika ndithu kwa anthuwo, koma sakubwerako ai.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anamuka wapakavalo kukomana naye, nati, Atero mfumu, Mtendere kodi? Nati Yehu, Ngwanji mtendere, tembenukira m'mbuyo mwanga. Ndi mlonda anawafotokozera kuti, Mthenga wawafika, koma wosabwera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho munthu wokwera kavalo anapita kukakumana ndi Yehu ndipo anati, “Mfumu ikufunsa kuti, ‘Kodi mukubwera mwamtendere?’ ” Yehu anayankha kuti, “Kodi iwe nkhani ya mtendere yakukhudza bwanji? Tiye, zinditsata pambuyo panga.” Mlonda uja anakafotokoza kwa mfumu kuti, “Wamthenga uja wakafika kwa anthuwo koma sakubwerera.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anamuka wapakavalo kukomana naye, nati, Atero mfumu, Mtendere kodi? Nati Yehu, Ngwanji mtendere, tembenukira m'mbuyo mwanga. Ndi mlonda anawafotokozera kuti, Mthenga wawafika, koma wosabwera.