2 Kings 9:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Yoramu adatumanso munthu wachiŵiri wokwera pa kavalo, amene adakafika kwa anthuwo nakaŵafunsanso kuti, “Mfumu ikufunsa kuti, ‘Kodi ndi zamtendere?’ ” Apo Yehu adayankhanso kuti, “Kodi iweyo nkhani ya mtendere uli nayo chiyani? Tiye, uzinditsata pambuyo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo anatumiza wina wapakavalo, nawafika, nati, Atero mfumu, Mtendere kodi? Nati Yehu, Ngwanji mtendere, tembenukira m'mbuyo mwanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho mfumu inatumanso munthu wina wachiwiri wokwera kavalo. Atafika kwa anthuwo iye anati, “Mfumu ikufunsa kuti, ‘Kodi mukubwera mwamtendere?’ ” Yehu anayankha kuti, “Kodi iwe nkhani ya mtendere yakukhudza bwanji? Tiye, zinditsata pambuyo panga.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo anatumiza wina wapakavalo, nawafika, nati, Atero mfumu, Mtendere kodi? Nati Yehu, Ngwanji mtendere, tembenukira m'mbuyo mwanga.