2 Kings 9:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mlonda uja adakanenanso kuti, “Amene ujanso wakafika kwa anthuwo, koma sakubwerako ai. Ndipo kuthamanga kwa mtsogoleri wa gululo nkoopsa, ndi ngati m'mene amathamangira Yehu mwana wa Nimisi.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi mlonda anafotokozera, kuti, Wawafika, koma wosabwera; ndipo kuyendetsako kukunga kuyendetsa kwa Yehu mwana wa Nimisi, pakuti ayendetsa moyaluka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mlonda uja anakanenanso kuti, “Wamthenga uja wakafika kwa anthuwo koma sakubwereranso. Kuyendako kukukhala ngati kwa Yehu mwana wa Nimisi, iye amayenda ngati munthu wamisala.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi mlonda anafotokozera, kuti, Wawafika, koma wosabwera; ndipo kuyendetsako kukunga kuyendetsa kwa Yehu mwana wa Nimsi, pakuti ayendetsa moyaruka.