2 Kings 9:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Atamva zimenezo Yoramu adati, “Konzekani.” Pomwepo anthuwo adakonza galeta lake. Tsono Yoramu mfumu ya ku Israele, pamodzi ndi Ahaziya mfumu ya ku Yuda, adanyamuka, wina m'galeta mwake, winanso mwake, ndipo adakumana ndi Yehu pa munda wa Naboti wa ku Yezireele uja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nati Yoramu, Manga. Namanga galeta wake. Ndipo Yoramu mfumu ya Israele ndi Ahaziya mfumu ya Yuda anatuluka yense m'galeta wake, natuluka kukakomana ndi Yehu, nakomana naye pa munda wa Naboti m'Yezireele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yoramu analamula kuti, “Konzani galeta langa.” Ndipo atakonza galeta lake, Yoramu mfumu ya Israeli ndi Ahaziya mfumu ya ku Yuda anakwera nʼkutuluka mu mzindamo, aliyense atakwera galeta lake, kukakumana ndi Yehu. Iwo anakumana ndi Yehu pa munda umene unali wa Naboti, wa ku Yezireeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nati Yoramu, Manga. Namanga gareta wace, Ndipo Yoramu mfumu ya Israyeli ndi Ahaziya mfumu ya Yuda anaturuka yense m'gareta wace, naturuka kukakomana ndi Yehu, nakomana naye pa munda wa Naboti m'Yezreeli.