2 Kings 9:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yoramu ataona Yehu, adafunsa kuti, “Iwe Yehu, kodi ndi zamtendere?” Iyeyo adayankha kuti, “Kodi pangakhale mtendere bwanji pamene za kupembedza mafano ndi zanyanga zimene adayamba mai wako zikupitirirabe?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali, pamene Yoramu anaona Yehu, anati, Mtendere kodi, Yehu? Nati iye, Ngwanji mtendere pokhala chachuluka chigololo ndi nyanga zake za mai wako Yezebele?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yoramu ataona Yehu anafunsa kuti, “Yehu, kodi wabwera mwamtendere?” Yehu anayankha kuti, “Pangakhale bwanji mtendere pamene zopembedza mafano zonse zilipo ndiponso ufiti wa amayi ako Yezebeli uli ponseponse?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunali, pamene Yoramu anaona Yehu, anari, Mtendere kodi, Yehu? Nati iye, Ngwanji mtendere pokhala cacuruka cigololo ndi nyanga zace za mai wako Yezebeli?