2 Kings 9:25 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pompo Yehu adauza Bidikari kapitao wake kuti, “Mnyamule, umponye m'munda wa Naboti wa ku Yezireele. Kumbukira kuti muja ine ndi iwe tinkayenda pambuyo pa Ahabu atate ake a Yoramu, Chauta adaamtemberera kuti,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nati Yehu kwa Bidikara kazembe wake, Mnyamule, numponye m'munda wa Naboti wa ku Yezireele; pakuti kumbukira m'mene ine ndi iwe tinali pa akavalo athu pamodzi kutsata Ahabu atate wake, Yehova anamsenzetsa katundu uyu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehu anawuza Bidikara, mtsogoleri wa galeta lake kuti, “Munyamule ndipo ukamuponye mʼmunda umene unali wa Naboti wa ku Yezireeli, chifukwa kumbukira mmene iwe ndi ine tinkayenda pambuyo pa Ahabu abambo ake, kuti Yehova ananeneratu za iye kuti,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nati Yehu kwa Bidikara kazembe wace, Mnyamule, numponye m'munda wa Naboti wa ku Yezreeli; pakuti kumbukila m'mene ine ndi iwe tinali pa akavalo athu pamodzi kutsata Ahabu atate wace, Yehova anamsenzetsa katundu uyu.