2 Kings 9:26 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
‘Ndithudi monga m'mene ndidaonera kuphedwa kwa Naboti ndi ana ake dzulo, ndikukuuza kuti Ine ndidzakubwezera choipa chimenechi pamunda pompano.’ Nchifukwa chake tsono, mtengeni, mumponye m'mundamu, potsata zimene Chauta adaanena.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndapenyadi dzulo mwazi wa Naboti ndi mwazi wa ana ake, ati Yehova; ndipo ndikubwezera pamunda pano, ati Yehova. Mtengeni tsono, mumponye pamundapo, monga mwa mau a Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
‘Zoonadi dzulo ndinaona magazi a Naboti ndi magazi a ana ake, akutero Yehova, ndipo Ine ndidzakubwezera ndithu choyipa chimenechi pa munda womwe uno, akutero Yehova.’ Tsono munyamule ndipo ukamuponye mʼmundamo, potsatira zimene Yehova ananena.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndapenyadi dzulo mwazi wa Naboti ndi mwazi wa ana ace, ati Yehova; ndipo ndikubwezera pamunda pano, ati Yehova, Mtengeni tsono, mumponye pamundapo, monga mwa mau a Yehova.