2 Kings 9:27 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Ahaziya mfumu ya ku Yuda ataona zimenezi, adathaŵira ku Betehagani. Koma Yehu adamlondola nati, “Nayenso mlaseni.” Ndipo adamlasira m'galeta pa chitunda cha Guri, pafupi ndi Ibleamu. Tsono Ahaziya adathaŵira ku Megido, nakafera komweko.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma pochiona ichi Ahaziya mfumu ya Yuda anathawa njira ya ku Betigahani. Namtsata Yehu, nati, Mumkanthe uyonso pagaleta; namkantha pa chikweza cha Guri chili pafupi pa Ibleamu. Nathawira iye ku Megido, namwalira komweko.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ahaziya mfumu ya ku Yuda ataona zimene zinachitika, anathawira ku Beti Hagani. Yehu anamuthamangitsa, uku akufuwula kuti, “Mupheninso!” Iwo anamuvulaza ali mʼgaleta lakelo pa njira yopita ku Guri pafupi ndi Ibuleamu, koma iye anathawira ku Megido ndipo anakafera kumeneko.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma pociona ici Ahaziya mfumu ya Yuda anathawa njira ya ku khumbi la m'munda. Namtsata Yehu, nati, Mumkanthe uyonso pagareta; namkantha pa cikweza ca Guru ciri pafupi pa Yibleamu. Nathawira iye ku Megido, namwalira komweko.