2 Kings 9:36 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Atabwererako anthuwo ndi kukamuuza Yehu, iyeyo adati, “Ameneŵa ndiwo mau a Chauta amene adalankhula kudzera mwa Eliya mtumiki wake wa ku Tisibe, kuti, ‘Agalu adzadya mtembo wa Yezibele ku dziko la Yezireele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nabwerera iwo, namfotokozera. Nati iye, Ndiwo mau a Yehova ananenawo mwa mtumiki wake Eliya wa ku Tisibe, ndi kuti, Pa munda wa Yezireele agalu adzadya mnofu wa Yezebele;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho iwo anabwerera kwa Yehu ndi kukamufotokozera kuti, “Mawu amene Yehova anayankhula kudzera mwa mtumiki wake Eliya wa ku Tisibe ndi awa: Pa munda wa ku Yezireeli agalu adzadya mtembo wa Yezebeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nabwerera iwo, namfotokozera. Nati iye, Ndiwo mau a Yehova ananena wo mwa mtumiki wace Eliya wa ku Tisibe, ndi koti, Pa munda wa Yezreeli agaru adzadya mnofu wa Yezebeli;