2 Kings 9:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Atafika, adapeza atsogoleri ankhondo ali pa msonkhano. Tsono iyeyo adati, “Zikomo bwana, ine ndili ndi mau oti ndikuuzeni.” Yehu adafunsa kuti, “Kodi ukunena yani mwa ifeyo?” Mneneri uja adayankha nati, “Inuyo bwana.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nalowa, ndipo taonani, akazembe a khamu alikukhala pansi; nati iye, Ndili ndi mau kwa inu, kazembe. Nati Yehu, Kwa yani wa ife tonse? Nati iye, Kwa inu, kazembe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atafika ku Giliyadiko anapeza atsogoleri a ankhondo ali pa msonkhano. Iye anati, “Mtsogoleri, ine ndili ndi uthenga wanu.” Ndipo Yehu anafunsa kuti, “Uthengawo ndi wa yani pakati pathu?” Mneneriyo anayankha kuti, “Ndi wa inuyo, mtsogoleri.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nalowa, ndipo taonani, akazembe a khamu alikukhala pansi; nati iye, Ndiri ndi mau kwa inu, kazembe. Nati Yehu, Kwa yani wa ife tonse? Nati iye, Kwa Inu, kazembe.