2 Kings 9:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo Yehuyo adanyamuka nakaloŵa m'nyumba. Ndipo mneneri uja adathira mafuta pamutu pa Yehu nati, “Chauta, Mulungu wa Israele, akuti akukudzozani inu kuti mukhale mfumu ya Aisraele, anthu a Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nanyamuka, nalowa m'nyumba; ndipo anatsanulira mafutawo pamutu pake, nanena naye, Atero Yehova Mulungu wa Israele, Ndakudzoza ukhale mfumu ya pa anthu a Yehova, ndiwo Aisraele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehu anayimirira nakalowa mʼnyumba. Pamenepo mneneriyo anakhuthulira mafuta pamutu pa Yehu ndipo ananena kuti, “Yehova Mulungu wa Israeli akuti, ‘Ine ndikukudzoza kukhala mfumu ya Israeli, anthu a Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nanyamuka, nalowa m'nyumba; ndipo anatsanulira mafutawo pamutu pace, nanena naye, Atero Yehova Mulungu wa Israyeli, Ndakudzoza ukhale mfumu ya pa anthu a Yehova, ndiwo Aisrayeli.