2 Kings 9:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono mukakanthe banja la Ahabu mbuyanu, kuti Chautayo alipsire Yezebele, chifukwa cha aneneri ake ndiponso atumiki ena onse amene iyeyo adaŵapha.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nudzakantha nyumba ya Ahabu mbuye wako, kuti ndibwezere chilango cha mwazi wa atumiki anga aneneri, ndi mwazi wa atumiki onse a Yehova, dzanja la Yezebele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Uyenera kuwononga nyumba ya mbuye wako Ahabu ndipo ndidzabwezera imfa ya atumiki anga, aneneri ndiponso imfa ya atumiki ena onse a Yehova amene anaphedwa ndi Yezebeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nudzakantha nyumba ya Ahabu mbuye wako, kuti ndibwezere cilango ca mwazi wa: atumiki anga aneneri, ndi mwazi wa atumiki onse a Yehova, dzanja la Yezebeli.