2 Peter 1:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iye adalandira ulemu ndi ulemerero kwa Mulungu Atate, ndipo adamufikira mau ochokera kwa Atate aulemererowo akuti, “Uyu ndi Mwana wanga wokondedwa, amene ndimakondwera naye.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti analandira kwa Mulungu Atate ulemu ndi ulemerero, pakumdzera Iye mau otere ochokera ku ulemerero waukulu, Uyu ndi Mwana wanga wokondedwa, amene Ine ndikondwera naye;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti Iye analandira ulemu ndi ulemerero kuchokera kwa Mulungu Atate atamufikira mawu ochokera ku ulemerero wa ukulu akuti, “Uyu ndi mwana wanga amene Ine ndimukonda, amene ndimakondwera naye kwambiri.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti analandira kwa Mulungu Atate ulemu ndi ulemerero, pakumdzera iye mao otere ocokera ku ulemerero waukuru, Uyu ndi Mwana wanga wokondedwa, amene Ine ndikondwera naye;