2 Peter 1:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo mau ameneŵa ifeifeyo tidaŵamva kuchokera kumwamba chifukwa tidaali naye pamodzi pa phiri loyera lija.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo mau awa ochokera Kumwamba tidawamva ife, pokhala pamodzi ndi Iye m'phiri lopatulika lija.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ifeyo tinamva mawuwa akuchokera kumwamba pamene tinali naye pamodzi pa phiri lopatulika lija.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo mau awa ocokera Kumwamba tidawamva ife, pokhala pamodzi ndi iye m'phiri lopatulika lija,