2 Peter 1:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero tikudziŵa ndithu tsopano kuti mau aja a anereriŵa ngoona. Nkwabwino tsono kuti muŵayang'anitsitse ngati nyale yoŵala m'malo amdima, kufikira nthaŵi imene kudzayambe kucha, pamene nyenyezi yam'mamaŵa idzayambe kuŵala m'mitima mwanu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo tili nao mau a chinenero okhazikika koposa; amene muchita bwino powasamalira, monga nyali younikira m'malo a mdima, kufikira kukacha, nikauka nthanda pa mtima yanu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono ifenso tili ndi mawu a uneneri amene ndi odalirika kwambiri ndipo inu mudzachita bwino mukawasamalira mawuwa, monga kuwunika kumene kukuwala mu mdima, mpaka tsiku lidzayambe kucha, pamene nthanda idzayambe kuwala mʼmitima mwanu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo tiri nao mau a cinenero okhazikika koposa; amene mucita bwino powasamalira, monga nyali younikira m'malo a mdima, kufikira kukaca, nikauka nthanda pa mtima yanu;