2 Peter 1:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mwa ulemerero ndi ubwino wakewo adatipatsa madalitso aakulu ndi amtengowapatali amene Iye adatilonjeza. Adatero kuti mulandireko moyo wake wa Mulungu, mutapulumuka ku chivunde chimene chili pa dziko lapansi chifukwa cha zilakolako zoipa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
mwa izi adatipatsa malonjezano a mtengo wake ndi akulu ndithu; kuti mwa izi mukakhale oyanjana nao umulungu wake, mutapulumuka kuchivundi chili pa dziko lapansi m'chilakolako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mwa ulemerero ndi ubwino wakewo, anatipatsa malonjezo opambana kwambiri ndi a mtengowapatali. Amenewa ndi malonjezo amene amakuthandizani kulandira nawo moyo wa Mulungu, titapulumuka ku chiwonongeko chimene chili mʼdziko lapansi chifukwa cha zilakolako zoyipa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
mwa izi adatipatsa malonjezano a mtengo wace ndi akuru ndithu; kuti mwa izi mukakhale oyanjana nao umulungu wace, mutapulumuka ku cibvundi ciri pa dziko lapansi m'cilakolako.