2 Peter 2:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Makamaka adzalanga anthu amene amatsata zilakolako zonyansa zathupi namanyoza ulamuliro. Aphunzitsi onyenga ndi odzikuza, osasamala munthu, saopa kuchita chipongwe aulemerero a Kumwamba.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
koma makamaka iwo akutsata za thupi, m'chilakolako cha zodetsa, napeputsa chilamuliro; osaopa kanthu, otsata chifuniro cha iwo eni, santhunthumira kuchitira mwano akulu aulemerero;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Makamaka amene amatsata zilakolako zonyansa zathupi nanyoza ulamuliro. Anthu amenewa ndi odzikuza, ndipo otsata chifuniro cha iwo eni, sasamala za munthu, saopa kuchitira chipongwe zolengedwa za mmwamba.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
kama makamaka iwo akutsata zathupi, m'cilakolako ca zodetsa, napeputsa cilamuliro; osaopa kanthu, otsata cifuniro ca iwo eni, santhunthumira kucitira mwano akulu;