2 Peter 2:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma anthu aŵa ali ngati nyama chabe, zolengedwa zopanda nzeru, zobadwira kuti zizigwidwa ndi kumaphedwa. Amanyoza mwachipongwe zinthu zosazidziŵa. Ndipo monga nyama zija, iwo omwe adzaonongedwa,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma awo, ngati zamoyo zopanda nzeru, nyama zobadwa kuti zikodwe ndi kuonongedwa, akuchitira mwano pa zinthu osazidziwa, adzaonongeka m'kuononga kwao,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma anthu awa amachita chipongwe zinthu zimene sakuzidziwa. Ali ngati zirombo zopanda nzeru. Zirombo zolengedwa kuti zigwidwe ndi kuwonongedwa, ndipo ngati zirombozo adzawonongedwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma awo, ngati zamoyo zopanda nzeru, nyama zobadwa kuti zikodwe ndi kuonongedwa, akucitira mwano pa zinthu osazidziwa, adzaonongeka m'kuononga kwao,