2 Peter 2:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
nadzalangidwa molingana ndi kuipa kwao. Chimene chimaŵakomera nkumangochita zokondweretsa thupi nthaŵi yamasana. Ali ngati mathotho ndi maŵanga onyansa, chifukwa podya nanu pamodzi amakondwera kuchita zonyenga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ochitidwa zoipa kulipira kwa chosalungama; anthu akuyesera chowakondweretsa kudyerera usana; ndiwo mawanga ndi zilema, akudyerera m'madyerero achikondi ao, pamene akudya nanu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo adzalangidwa chifukwa cha zoyipa zimene anachita. Koma chimene chimawakomera ndi kumangochita zokondweretsa thupi masanasana. Iwo ali ngati mawanga ndi zilema. Podya nanu pamodzi amakondwera kuchita za chinyengo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ocitidwa zoipa kulipira kwa cosalungama; anthu akuyesera cowakondweretsa kudyerera usana; ndiwo mawanga ndi zirema, akudyerera m'madyerero acikondi ao, pamene akudya nanu;