2 Peter 2:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mulungu sadaŵalekererenso anthu akale aja, koma adangosunga Nowa yekha, mlaliki wa chilungamo, pamodzi ndi anzake asanu ndi aŵiri, pamene adadzetsa chigumula pa dziko la anthu osasamala za Iye Mulunguyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo sanalekerera dziko lapansi lakale, koma anasunga Nowa mlaliki wa chilungamo, ndi anzake asanu ndi awiri, pakulitengera dziko la osapembedza chigumula;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye sanalekerere dziko lapansi kalelo, koma anapulumutsa Nowa, mlaliki wa chilungamo, ndi anthu ena asanu ndi awiri atadzetsa chigumula pa dziko lapansi kwa anthu akhalidwe losapembedza Mulunguyo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo sanalekerera dziko lapansi lakale, koma anasunga Nowa mlaliki wa cilungamo, ndi anzace asanu ndi awiri, pakulitengera dziko la osapembedza cigumula;