2 Peter 2:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndiponso Mulungu adaweruza mzinda wa Sodomu ndi wa Gomora naiwononga ndi moto, kuti chimenechi chikhale chitsanzo chochenjeza anthu amene adzakhale osasamala za Mulungu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo pakuisandutsa makala midzi ya Sodomu ndi Gomora anaitsutsa poigwetsa, ataiika chitsanzo cha kwa iwo akakhala osapembedza;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mulungu anaweruza mizinda ya Sodomu ndi Gomora nayiwononga ndi moto, kuti ikhale chitsanzo cha zimene zidzachitikira anthu osapembedza Mulungu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo pakuisandutsa makara midzi ya Sodoma ndi Gomora anaitsutsa poigwetsa, ataiika citsanzo ca kwa iwo akakhala osapembedza;