2 Peter 2:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Munthu wolungama uja, pokhala pakati pao, analikumva ndi kuwona machitidwe ao oipa, ndipo tsiku ndi tsiku mtima wake wolungama unkavutikadi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
(pakuti wolungamayo pokhala pakati pao. Ndi kuona ndi kumva zao, anadzizunzira moyo wake wolungama tsiku ndi tsiku ndi ntchito zao zosaweruzika).
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
(Pakuti munthu wolungamayo, pokhala pakati pawo tsiku ndi tsiku ankavutika mu mtima ndi makhalidwe awo oyipa amene ankawaona ndi kuwamva).
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
(Pakuti wolungamayo pokhala pakati pao, ndi kuona ndi kumva zao, anadzizunzira moyo wace wolungama tsiku ndi tsiku ndi nchito zao zosayeruzika).