2 Peter 3:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma potsata lonjezo la Mulungu, tikudikira kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano, m'mene chilungamo chizidzakhalamo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma monga mwa lonjezano lake tiyembekezera miyamba yatsopano, ndi dziko latsopano m'menemo mukhalitsa chilungamo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma ife tikudikira kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano, zimene Mulungu analonjeza, mʼmene chilungamo chidzakhalamo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma monga mwa lonjezano lace tiyembekezera miyamba yatsopano, ndi ziko latsopano m'menemo mukhalitsa cilungamo.