2 Peter 3:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Paja amanena chimodzimodzi m'makalata ake onse polemba za zimenezi. M'makalatamo muli zina zapatali kuzimvetsa, ndipo anthu osaphunzira ndi a nzeru zosakhazikika amazipotoza, monga amapotozeranso Malembo ena. Pakutero akungodziwononga okha.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
monganso m'akalata ake onse pokamba momwemo za izi; m'menemo muli zina zovuta kuzizindikira, zimene anthu osaphunzira ndi osakhazikika apotoza, monganso atero nao malembo ena, ndi kudziononga nao eni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye walemba chimodzimodzi makalata ake onse, kuyankhula za zinthu izi. Mʼmakalata ake mumakhala zinthu zina zovuta kuzimvetsa, zimene anthu osadziwa ndi osakhazikika amazipotoza, monga amachita ndi malemba ena onse, potero akudziwononga okha.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
monganso m'akalata ace onse pokanba momwemo za izi; m'menemo nuli zina zobvuta kuzizindikira, zinene anthu osaphunzira ndi osachazikika apotoza, monganso atero lao malembo ena, ndi kudziononga lao eni.