2 Samuel 1:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho ndidasendera pafupi, nkumupha, poti ndidaadziŵa kuti akagwa, sakhala moyo. Tsono ndidamuvula chisoti chaufumu kumutu kwake ndi chigwinjiri kumkono kwake, ndipo ndabwera nazo kuno kwa inu mbuyanga.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
M'mwemo ndinakhala pambali pake ndi kumtsiriza chifukwa ndinadziwa kuti sangakhalenso ndi moyo wake, atagwa. Ndipo ndinatenga korona wa pamutu pake, ndi chigwinjiri cha pa mkono wake, ndabwera nazo kuno kwa mbuye wanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Kotero ndinabwera pafupi ndi kumupha, chifukwa ndinadziwa kuti mmene anagweramo sakanakhalanso ndi moyo. Ndipo ndatenga chipewa chaufumu chimene chinali pamutu pake ndi khoza la pa dzanja lake ndipo ndazibweretsa kwa inu mbuye wanga.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
M'mwemo ndinakhala pambali pace ndi kumtsiriza cifukwa ndinadziwa kuti sangakhalenso ndi moyo wace, atagwa. Ndipo ndinatenga korona wa pamutu pace, ndi cigwinjiri ca pa mkono wace, ndabwera nazo kuno kwa mbuye wanga.