2 Samuel 1:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo anthuwo adabuma maliro. Adalira ndi kusala zakudya mpaka madzulo chifukwa cha Saulo ndi Yonatani mwana wake. Adaliranso chifukwa cha Aisraele, anthu a Chauta, chifukwa choti anali ataphedwa ku nkhondo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nabuma, nalira misozi, nasala kudya kufikira madzulo, chifukwa cha Saulo ndi mwana wake Yonatani, ndi anthu a Yehova, ndi banja la Israele, chifukwa adagwa ndi lupanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo analira maliro ndi kusala zakudya mpaka madzulo chifukwa cha Sauli ndi mwana wake Yonatani, komanso chifukwa cha gulu la ankhondo la Yehova ndi nyumba ya Israeli, chifukwa anaphedwa ndi lupanga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nabuma, nalira misozi, nasala kudya kufikira madzulo, cifukwa ca Sauli ndi mwana wace Jonatani, ndi anthu a Yehova, ndi banja la Israyeli, cifukwa adagwa ndi lupanga.