2 Samuel 1:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pomwepo Davide adaitana mmodzi mwa ankhondo ake, namuuza kuti, “Mtenge ameneyu, ukamuphe.” Wankhondoyo adamkanthadi naafa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Davide naitana wina wa anyamatawo, nati, Sendera numkanthe. Ndipo anamkantha, nafa iye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka Davide anayitana mmodzi mwa anyamata ake ndipo anati, “Pita ukamukanthe!” Kotero iye anapita kukamukantha, ndipo mnyamata uja anafa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Davide naitana wina wa anyamatawo, nati, Sendera numkanthe, Ndipo anamkantha, nafa iye.