2 Samuel 1:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono pa tsiku lachitatu lake, adangoona munthu akuchokera ku zithando zankhondo za Saulo, atavala zovala zong'ambika ndiponso atadzithira dothi kumutu. Munthuyo atafika kwa Davide, adadzigwetsa pansi, namlambira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
pa tsiku lachitatu, onani, munthu anatuluka ku zithando za Saulo, ali ndi zovala zake zong'ambika, ndi dothi pamutu pake; ndipo kunatero kuti iye, pofika kwa Davide, anagwa pansi namgwadira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa tsiku lachitatu munthu wina wochokera ku msasa wa Sauli anafika, zovala zake zitangʼambika ndiponso anali atathira dothi pamutu pake. Atafika kwa Davide, anadzigwetsa pansi, kupereka ulemu kwa Davideyo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
pa tsiku lacitatu, onani, munthu anaturuka ku zithando za Sauli, ali ndi zobvala zace zong'ambika, ndi dothi pamutu pace; ndipo kunatero kuti iye, pofika kwa Davide, anagwa pansi namgwadira.